Numbers 21:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Aisraele adapha Ogi, ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalira, ndipo adalanda dziko lakelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake amuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Aisraeli anapha Ogi pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse la nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala wamoyo, ndipo analanda dziko lakelo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamkantha iye, ndi ana ace amuna ndi anthu ace onse, kufikira sanatsala ndi mmodzi yense; nalanda dziko lace likhale lao lao.