Numbers 21:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kuticotsa ku Aigupto kuti tifere m'cipululu? pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wacabe uwu.