Numbers 21:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthu adabwera kwa Mose, namuuza kuti, “Pepani tidachimwa poti tidakangana ndi Chauta ndi inu nomwe. Mupemphere kwa Chauta kuti atichotsere njokazi.” Choncho Mose adaŵapempherera anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tacimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti aticotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.