Numbers 21:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Mose adapanga njoka yamkuŵa, naipachika pa mtengo. Ndiye ankati wina aliyense njoka ikamuluma, munthuyo akayang'ana njoka yamkuŵa ija, ankakhala moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa ndi kuyipachika pa mtengo. Ndipo aliyense wolumidwa akayangʼana njoka yamkuwayo ankakhala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu ali yense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.