Numbers 22:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Anthu amene achokera ku Ejipito, adzaza dziko lonse. Bwerani tsono, muŵatemberere m'malo mwanga, mwina mwake ndidzatha kumenyana nawo nkhondo ndi kuŵapirikitsa.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, anthu awa adatuluka m'Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, anthu awa adaturuka m'Aigupto aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapitikitsa.