Numbers 22:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Balamu adayankha atumiki a Balakiwo kuti, “Ngakhale Balaki akadati andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindikadatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta, Mulungu wanga, wandilamula. Sindikadatha kuchepetsa kapena kuwonjeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Balaamu anayankha atumiki a Balaki kuti, “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingachite chilichonse chachikulu kapena chachingʼono kuposa kuchita lamulo la Yehova Mulungu wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Balamu, anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Cinkana Balaki andipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kucepsako kapena kuonjezako.