Numbers 22:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu usiku umenewo namuuza kuti, “Ngati anthuwo abwera kudzakuitana, nyamuka upite nao. Koma ukachite zokhazo zimene ndikakulamule.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usiku umenewo Mulungu anabwera kwa Balaamu ndipo anati, “Popeza anthu awa abwera kudzakuyitana, nyamuka, pita nawo koma ukachite zokhazo zimene ndikuwuze.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kumka nao, koma mau okha okha ndinena ndi iwe, ndiwo ukacite.