Numbers 22:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bulu uja adaona mngelo wa Chauta ataima mu mseu, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono bulu adasiya mseu nakaloŵa m'munda. Apo Balamu adammenya bulu uja kuti abwerere mu mseu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene buluyo anaona mngelo wa Yehova atayima pa njira ndi lupanga mʼmanja mwake, anapatukira kumbali kwa msewu napita kutchire. Balaamu anamumenya kuti abwerere mu msewu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo buruyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lace ku dzanja lace; ndi buru anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda buru kumbwezera kunjira.