Numbers 22:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mngelo wa Chauta uja adakaimirira m'kanjira kophaphatiza, kodzera pakati pa minda yamphesa, kokhala ndi khoma pa mbali zonse ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mngelo wa Yehova anayima mʼkanjira kakangʼono pakati pa minda iwiri ya mpesa yokhala ndi makoma mbali zonse
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali yina kuli linga, mbali yina linga.