Numbers 22:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adadzipanikiza ku khoma, nakanikiza phazi la Balamu kukhomako. Pomwepo Balamu adamenya buluyo kachiŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bulu uja ataona mngelo wa Yehova anadzipanikiza ku khoma, kukhukhuza phazi la Balaamu kukhomako. Ndipo pomwepo Balaamu anamenya buluyo kachiwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo buru anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.