Numbers 22:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adagona pansi, Balamu ali pamsana pake. Balamu adapsa mtima kwambiri, namenya buluyo ndi ndodo yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anagona pansi Balaamu ali pa msana, ndipo iye anakwiya ndi kumumenya ndi ndodo yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo buru wace anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pace; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda buru ndi ndodo.