Numbers 22:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mngelo wa Chauta adauza Balamu kuti, “Pita nawo anthuŵa. Koma ukanene zokhazo zimene ndikakuuze.” Choncho Balamu adapitirira ulendo wake pamodzi ndi akalonga a Balaki aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okha okha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene, Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.