Numbers 22:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Balaki atamva kuti Balamu wafika, adatuluka kukamchingamira ku mzinda wina wokhala pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, umene umachita malire a dziko la Mowabu, kumapeto kwake kwenikweni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumudzi wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Balaki atamva kuti Balaamu akubwera, anapita kukakumana naye ku mzinda wa Mowabu umene unali mʼmalire a Arinoni, mʼmphepete mwa dziko lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamturukira kukakomana naye ku mudzi wa Moabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ace.