Numbers 22:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Amowabuwo adauza akuluakulu a ku Midiyani kuti, “Tsopano khamu limeneli libudula zonse zimene zatizungulira, monga momwe ng'ombe zimabudulira udzu wam'munda.” Pamenepo Balaki mwana wa Zipori amene anali mfumu ya Mowabu nthaŵi imeneyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.” Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Moabu anati kwa akuru a Midyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse ziri pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Moabu masiku amenewo.