Numbers 22:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adatuma amithenga kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate m'dziko la kwao, kuti akamuitane ndi kumuuza kuti, “Anthu ochokera ku Ejipito adzaza dziko lonse, ndipo akuyang'anana ndi ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m'dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anatumiza amithenga kwa Balaamu mwana wa Beori, yemwe anali ku Petori, pafupi ndi mtsinje, mʼdziko la kwawo kuti akamuyitane. Balaki anati: “Taonani, anthu ochokera ku Igupto abwera, adzaza dziko lonse ndipo akufuna kuchita nane nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wace, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anaturuka anthu m'dziko la Aigupto; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.