Numbers 22:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bwerani tsono muŵatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga, poti ngamphamvu kopambana ine. Mwina mwake ndidzatha kuŵagonjetsa ndi kuŵapirikitsa m'dziko mwanga. Pakuti ndikudziŵa kuti amene inu mumamdalitsa, amadalitsidwa, ndipo amene mumamtemberera, amatembereredwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawalaka, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapitikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.