Numbers 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho akalonga a ku Mowabu ndi akalonga a ku Midiyani adanyamuka, atatenga ndalama m'manja zokaombedzera. Tsono adafika kwa Balamu namuuza mau a Balaki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru a Moabu ndi akuru a Midyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.