Numbers 22:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Balamu adaŵauza kuti, “Gonani konkuno lero, ndipo ndikubwezerani mau monga momwe Chauta andiwuzire.” Choncho akalonga a ku Mowabu adagona kwa Balamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Balaamu anawawuza kuti, “Mugone konkuno usiku uno, ndipo ndikuyankhani zomwe Yehova andiwuze.” Choncho akuluakulu a Amowabu anagona kwa Balaamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Moabu anagona ndi Balamu.