Numbers 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani angathe kuŵerenga zidzukulu, zidzukulu za Yakobe zochuluka ngati fumbi, kapena kuŵerenga ngakhale chimodzi mwa zigawo zinai za fuko lonse la Israele? Lekeni ine ndife imfa ya anthu amene mudaŵalungamitsa, matsiriziro anga akhale onga a anthu amenewo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzawerenga ndani fumbi la Yakobo, kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israele? Ndipo ine ndife monga amafa oongoka mtima, chitsiriziro changa chifanane nacho chake!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani angawerenge zidzukulu za Yakobo zochuluka ngati fumbi, kapena chimodzi mwa zigawo zinayi za Israeli? Lekeni ndife imfa ya oyera mtima, ndi chimaliziro changa chikhale ngati chawo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzawerenga ndani pfumbi la Yakobo, Kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israyeli? Ndipo ine ndife monga amafa aongoka mtima, Citsiriziro canga cifanane naco cace!