Numbers 23:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapita naye ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga, namangapo maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo adapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi nsembe ya nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa pa guwa la nsembe liri lonse.