Numbers 23:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adabwerera kwa Balaki, ndipo adangoona akuimirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, ali ndi akalonga a ku Mowabu aja. Balaki adamufunsa kuti, “Nanga Chauta wakuuzani zotani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yace yopsereza, ndi akalonga a Moabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?