Numbers 23:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu sali ngati munthu kuti angathe kunama, si munthu kuti angathe kusintha maganizo ake. Kodi sadzachitadi zomwe adanena? Kapena sadzachitadi zimene adalankhula?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu si munthu kuti aname, kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake. Kodi amayankhula koma osachita? Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; Kapena mwana wa munthu, kuti aleke; Kodi anena, osacita?