Numbers 23:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye sadaone choipa mwa Yakobe, sadaone chovuta mwa Israele. Chauta wao ali nawo, ndipo pakati pao pali kufuula kuti Iye ndi mfumu yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sayang'anira mphulupulu ili m'Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli m'Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo, sanaone chovuta mu Israeli. Yehova Mulungu wawo ali nawo: mfuwu wa mfumu uli pakati pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sayang'anira mphulupulu iri m'Yakobo, Kapena sapenya kupulukira kuli m'lsrayeli. Yehova Mulungu wace ali ndi iye, Ndi mpfuu wa mfumu uli pakati pao,