Numbers 23:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani Aisraele, kudzuka kwanu kuli ngati kwa mkango waukazi, kudzambatuka kwanu kuli ngati kwa mkango waumuna, umene sugona pansi mpaka utagwira nyama ndi kuidya ndi kumwa magazi ake a nyama yojiwayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, anthu anyamuka ngati mkango waukazi; adzuka okha ngati mkango waumuna umene supuma mpaka utadya nyama imene wagwira ndi kumwa magazi a nyama yogwidwayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, Nadzitukumula ngati mkango waumuna: Sugonansokufikira utadya nyama yogwira, Utamwa mwazi wa zophedwa.