Numbers 23:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Balamu adauza Balaki kuti, “Imani pafupi ndi nsembe yanu yopsereza, tsono ine ndipite, mwina mwake Chauta abwera kudzakumana nane. Chilichonse chimene andiwonetse ndidzakuuzani.” Choncho adapita pamwamba pa phiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo cimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera,