Numbers 23:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Balaki mfumu ya ku Mowabu yandiitana kuchokera ku Aramu, ku mapiri akuvuma, kuti, ‘Bwerani, dzatemberereni Yakobe m'malo mwanga, bwerani mudzamfunire Israele zoipa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Balaamu ananena uthenga wake: “Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu, mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa. Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga, pita nyoza Israeli.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena fanizo lace, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, Mfumu ya Moabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa; Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israyeli.