Numbers 24:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Balamu adaona kuti zinali zokondwetsa Chauta kuti adalitse Aisraele, sadapite monga nthaŵi zina zija kukafunsa kuti adziŵe zimene Mulungu akufuna, koma adangotembenuka nayang'ana ku chipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yake kuchipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israyeli, sanamuka, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yace kucipululu.