Numbers 24:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Balaki adapsera mtima Balamu, ndipo adaomba m'manja. Tsono Balakiyo adauza Balamu kuti, “Paja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, ndipo inu mwaŵadalitsa katatu konseka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani ansa, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.