Numbers 24:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Ngakhale Balaki andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindidzatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta wandiwuza. Sindidzachita zabwino kapena zoipa mwa kufuna kwanga. Ndidzalankhula zimene Chauta adzandiwuze?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cinkana Balaki akandipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kucita cokoma kapena coipa ine mwini wace; conena Yehova ndico ndidzanena ine?