Numbers 24:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
munthu amene akumva mau a Mulungu, ndipo akudziŵa nzeru zake za Wopambanazonse, munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya, munthu amene akugwa pansi, koma maso ake ali chipenyere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba, amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anenetsa wakumva mau a Mulungu, Ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, Wakugwa pansi wopenyuka maso;