Numbers 24:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikupenya mtsogolo, ndipo ndikuona mtundu wa Israele. Mfumu yonga nyenyezi idzatuluka mwa Yakobe, ndodo yaufumu idzadzuka mwa Israele, idzatswanya atsogoleri a Mowabu, ndipo idzagonjetseratu mtundu wa Seti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi m'Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka m'Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndikumuona iye koma osati tsopano; ndikumupenya iye koma osati pafupi. Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo; ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli. Iye adzagonjetsa Mowabu ndi kugonjetsa ana onse a Seti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndimuona, koma tsopano ai; Ndimpenya, koma si pafupi ai; Idzaturuka nyenyezi m'Yakobo, Ndi ndodo yacifumu idzauka m'Israyeli, Nidzakantha malire a Moabu, Nidzapasula ana onse a Seti,