Numbers 24:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Balamu adayang'ana Amaleke, ndipo adayamba kulankhula nati, “Mtundu wa Amaleke udaali wopambana mitundu ina yonse, koma potsiriza pake udzaonongeka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu: “Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu koma potsiriza pake adzawonongeka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayang'ana ku Amaleki, nanena fanizo lace, nati, Amaleki ndiye woyamba wa amitundu; Koma citsiriziro cace, adzaonongeka ku nthawi zonse.