Numbers 24:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ali ndi mphamvu zonga za njati, adzapha mitundu ya adani ao, adzaswa mafupa ao ndi kuŵaboola ndi mivi yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu amtulutsa m'Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto ali ndi mphamvu ngati za njati. Amawononga mitundu yomuwukira ndi kuphwanya mafupa awo, amalasa ndi mivi yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu amturutsa m'Aigupto; Ali nayo mphamvu yonga ya njati; Adzawadya amitundu, ndiwo adani ace. Nadzaphwanya mafupa ao, Ndi kuwapyoza ndi mibvi yace.