Numbers 24:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamyata, nagona pansi ngati mkango ngati mkango wamphongo kapena waukazi. Kodi amuutse ndani? Ndi wodala munthu amene aŵadalitsa, ndi wotembereredwa munthu amene aŵatemberera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anauthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi, monga mkango waukazi, adzamuputa ndani? “Amene adalitsa iwe, adalitsike ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaunthama, nagona pansi ngati mkango, Ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika ali yense wakudalitsa iwe, Wotemberereka ali yense wakutemberera iwe.