Numbers 25:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, wandiletsa kuti ndisaŵaononge Aisraele, chifukwa choti sadalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine, nchifukwa chake sindidaŵaononge ndili wokwiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israele m'nsanje yanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israyeli, popeza anacita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israyeli m'nsanje yanga.