Numbers 25:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikupangana naye iyeyu ndi zidzukulu zake zonse, chipangano cha unsembe wamuyaya, chifukwa sadalole kuti anthu aukire Ine Mulungu, ndipo adachita ntchito yopepesera machimo a Aisraele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikupangana naye pangano la unsembe wosatha, iyeyo pamodzi ndi zidzukulu zake zonse, chifukwa sanalole kuti anthu awukire Ine Mulungu, ndipo anachita ntchito yopepesera machimo Aisraeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zace zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anacita nsanje cifukwa ca Mulungu wace, anawacitira ana a Israyeli cowatetezera.