Numbers 25:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
chifukwa choti adakuchitani zachabe pokunyengani ku Peori, ndiponso chifukwa cha nkhani ya mlongo wao Kozibi, mwana wamkazi wa mfumu ya ku Midiyani, amene adaphedwa pa nthaŵi ya mliri chifukwa cha zochitika ku Peori zija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'chija cha Peori.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa ankakuonani inu ngati adani awo pamene anakupusitsani pa nkhani ya ku Peori, ndiponso za mlongo wawo Kozibi, mwana wamkazi wa mtsogoleri wa Amidiyani, mkazi yemwe anaphedwa pamene mliri unabwera chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'cija ca Peori, ndi ca Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'cija ca Peori.