Numbers 26:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa, anthu okwanira 32,500, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a ana aamuna a Efuremu, zidzukulu za Yosefe potsata mabanja ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo ndiwo mabanja a ana a Efraimu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.