Numbers 26:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Potsata mabanja ao ana aamuna a Dani anali aŵa: Suhamu anali kholo la banja la Asuhamu. Ameneŵa ndiwo mabanja a Dani potsata mabanja ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ake ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu. Izi zinali zidzukulu za Dani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ace ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.