Numbers 26:59 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi wa Amuramu anali Yokebede mwana wa Levi, amene adabadwira ku Ejipito. Yokebedeyo adamubalira Amuramu ana aŵa: Aroni, Mose ndi Miriyamu mlongo wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzina lace la mkazi wace wa Amiramu ndiye Yokebedi, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Aigupto; ndipo iye anambalira Amiramu Aroni ndi Mose, ndi Miriamu mlongo wao.