Numbers 26:62 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene adaŵerengedwa mwa Aleviwo anali 23,000, kuyambira ana aamuna a mwezi umodzi ndi opitirirapo. Iwowo sadaŵaŵerengere kumodzi ndi Aisraele, chifukwa sadapatsidwe choloŵa pakati pa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwa pakati pa ana a Israyeli; cifukwa sanawapatsa colowa mwa ana a Israyeli.