Numbers 26:64 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pakati pa anthu ameneŵa panalibe ndi mmodzi yemwe wamoyo amene adaaŵerengedwa kale ndi Mose ndi wansembe Aroni, pamene ankaŵerenga Aisraelewo ku chipululu cha Sinai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israyeli m'cipululu ca Sinai.