Numbers 26:65 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja za iwowo Chauta adati, “Adzafera m'chipululu.” Sadatsale ndi mmodzi yemwe mwa iwo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'cipululu. Ndipo sanatsalira mmodzi wa iwowa koma Kalebi mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.