Numbers 27:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo kudabwera ana aakazi a Zelofehadi. Iyeyo anali mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, a m'mabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana ake aakaziwo anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anayandikiza ana akazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wamwamuna wa Manase, a mʼmabanja a Manase, mwana wa Yosefe anabwera. Mayina a ana aakaziwo anali awa: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anakayima
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anayandikiza ana akazi a Tselofekadi mwana wa Heferi, ndiye mwana wa Gileadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ace akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.