Numbers 27:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bambo wakeyo akakhala wopanda abale, choloŵa chakecho upatse wachibale wake pabanja pakepo, ndipo chidzakhala chake. Ameneŵa akhale malamulo ndi malangizo kwa Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akapanda abale a atate wake, mupatse wa chibale chake woyandikizana naye wa fuko lake cholowa chake, likhale lakelake; ndipo likhale kwa ana a Israele lemba monga Yehova wamuuza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akapanda abale a atate wace, mupatse wa cibale cace woyandikizana naye wa pfuko lace colowa cace, likhale lace lace; ndipo likhale kwa ana a Israyeli lemba monga Yehova wamuuza Mose.