Numbers 27:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adzapite kwa wansembe Eleazara amene adzamdziŵitse zimene Chauta akufuna, pofunsa kwa Urimu ndi Tumimu. Umotu ndi m'mene Iyeyu adzatsogolere ndi kulamula Yoswa ndi mpingo wonse wa Aisraele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayime pamaso pa wansembe Eliezara, amene adzamudziwitse zimene Yehova akufuna pogwiritsa ntchito Urimu. Iye akalamula, Aisraeli onse azituluka ndipo akalamulanso, Aisraeliwo azibwereranso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa ciweruzo ca Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituruka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israyeli pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.