Numbers 27:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ana aakazi a Zelofehadiwo akunena zoona. Uŵapatse choloŵa chao pakati pa abale a bambo wao. Uŵapatse choloŵa cha bambo waocho kuti chikhale chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana akazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana akazi a Tselofekadi anena zaona; uwapatse ndithu colowa cikhale cao cao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse colowa ca atate wao.