Numbers 28:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chopereka cha chakudya ikhale ya ufa wosalala wa makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, pa ng'ombe yamphongo iliyonse. Muperekenso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yamphongoyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iri yonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo;