Numbers 28:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiponso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza yotulutsa fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwanawankhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwana wa nkhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya pfungo lokoma, nsembe yamoto ya. Yehova.