Numbers 28:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chopereka cha chakumwa chikhale cha vinyo wokwanira malita aŵiri pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ya vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka pa nkhosa yamphongoyo, ndi ya vinyo wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse, pa miyezi yonse ya chaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nsembe zace zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la bini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwana wa nkhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uli wonse kunena miyezi yonse ya caka.